Mtumwi Mateyu akutiuza ife kuti Mau a Yesu analankhulidwa kwa aliyense m'dziko lino, popeza Iye ankaona Yesu monga Mfumu ya mafumu. Tsopano, Akristu dziko lonse lapansi, amene angobadwa mwatsopano pokhulupilira mu uthenga wabwino wa madzi ndi Mzimu omwe tikufalitsa, indedi akufunitsitsa kudya mkate wamoyo. Koma ndikobvuta kwa iwo kukhala ndi chiyanjano ndi ife mu uthenga wabwino weni weni, popeza iwo onse ali kutali ndi ife. Choncho, kuti tikumane ndi zofunika zauzimu za anthu amenewa a Yesu Kristu, Mfumu ya mafumu, ulaliki m'buku limeneli wakonzedwa monga mkate watsopano wa moyo kwa iwo kuti usamalire kukula kwao kwauzimu. Mlembi amanena kuti iwo amene alandira chikhululukiro cha machimo ao pokhulupilira m'Mau a Yesu Kristu, Mfumu ya mafumu, ayenera kudya Mau Ake angwiro pofuna kuteteza chikhulupiliro chao komanso kuchita bwino m'miyoyo yao yauzimu. Buku limeneli lidzapereka mkate weni weni wamoyo wauzimu kwa inu nonse amene mwakhala anthu olemekezeka a Mfumu mwa chikhulupiliro. Kudzera mu Mpingo Wake ndi akapolo Ake, Mulungu adzapitiriza kupereka kwa inu mkate umenewu wamoyo. Lolani madalitso a Mulungu akhale pa inu nonse amene mwabadwa mwatsopano mwa madzi ndi Mzimu, amene mukufuna kukhala ndi chiayanjano chauzimu ndi ife mwa Yesu Kristu.
Dieser Download kann aus rechtlichen Gründen nur mit Rechnungsadresse in A, B, CY, CZ, D, DK, EW, E, FIN, F, GR, H, IRL, I, LT, L, LR, M, NL, PL, P, R, S, SLO, SK ausgeliefert werden.